Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:6 - Buku Lopatulika

6 Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:6
18 Mawu Ofanana  

Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo;


Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao.


Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya.


ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.


Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.


pakuti Mombolo wao walimba; adzawanenera mlandu wao pa iwe.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;


koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu.


ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.


Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.


Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.


Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa