Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 9:7 - Buku Lopatulika

7 Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 9:7
17 Mawu Ofanana  

Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.


Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.


Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndi siliva, ndi mkuwa;


Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.


Mwini diso lamataya adzadala; pakuti apatsa osauka zakudya zake.


Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.


koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafune kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.


Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa