Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 107:2 - Buku Lopatulika

2 Atere oomboledwa a Yehova, amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Atere oomboledwa a Yehova, amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anenedi choncho oomboledwa a Chauta, amene Iye waŵapulumutsa ku mavuto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Owomboledwa a Yehova anene zimenezi amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 107:2
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani.


Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse.


Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu; mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa choonadi.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m'menemo;


Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mzinda wosasiyidwa.


Pakuti tsiku lakubwezera lili mumtima mwanga, ndi chaka cha kuombola anthu anga chafika.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu.


Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha,


Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi.


Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya ukapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa