Masalimo 112 - Buku LopatulikaAdalitsidwa akuopa Mulungu 1 Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. 2 Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa. 3 M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire. 4 Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama. 5 Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa. 6 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha. 7 Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova. 8 Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa. 9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu. 10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi