Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 112:8 - Buku Lopatulika

8 Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ali wolimba mtima, sadzachita mantha, potsiriza adzaona adani ake atagonja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 112:8
11 Mawu Ofanana  

Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?


Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.


Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.


Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.


Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.


Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao;


Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira, adzandionetsa tsoka la adani anga.


Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa.


Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira.


Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama.


Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa