Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 112:10 - Buku Lopatulika

10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 112:10
15 Mawu Ofanana  

Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.


koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake; iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye?


Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.


Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.


Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.


Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.


Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka; chiyembekezo cha uchimo chionongeka.


Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.


koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.


Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa