Masalimo 100 - Buku LopatulikaOlengedwa ndi Mulungu amlemekeze Salimo la Chiyamiko. 1 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. 2 Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera. 3 Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake. 4 Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. 5 Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi