Masalimo 126 - Buku LopatulikaAyamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo wao Nyimbo yokwerera. 1 Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota. 2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu. 3 Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera. 4 Bwezani ukapolo wathu, Yehova, ngati mitsinje ya kumwera. 5 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. 6 Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi