Masalimo 126:2 - Buku Lopatulika2 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.” Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.