Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 43:4 - Buku Lopatulika

4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana. Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. Ndidzakutamandani ndi zeze, Inu Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 43:4
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.


Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi.


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa.


Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu.


Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.


Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka, zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa