Mukudziwa, Mulungu ndi Atate wabwino kwambiri. Amadziwa zomwe tikufunikira ngakhale tisanapemphe. Koma amafuna kuti timupemphe. Mukampempha Mulungu, mukuvomereza kuti simungathe kuchita zinthu paokha. Zili ngati mukutsegula mtima wanu kwa Iye.
Kaya mukufunikira chakudya, chitetezo, machiritso, kapena malangizo, muuzeni Atate wanu wakumwamba. Musachite manyazi. Monga momwe lemba la Masalmo 139:4 limati, “Ambuye, Inu mundidziwa bwino lomwe; mundidziwa ine ndisanayambe kulankhula.”
Pemphero ndiye chinsinsi chotsegulira chuma cha Ufumu wa Mulungu. Mulungu wapereka chinsinsi chimenechi m'manja mwanu. Taganizirani izi: Mulungu ndiye mwini zonse. Angathe kungotipatsa zomwe tikufunikira popanda kupempha. Koma sakuchita zimenezo.
Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amatikonda ndipo amafuna kuti tizilankhulana naye. Amafuna ubwenzi weniweni ndi ife. Pemphero ndi njira imene madalitso ake amatifiikira. Ndipo ndi njira imene timamudziwira bwino.
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu.
Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera. Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse: Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.
Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga. Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.
Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.
Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.
Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.
Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake. Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova; mundizindikiritse monga mwa mau anu.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. Khulupirirani Yehova nthawi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.
Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku. Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.
Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga. Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu. Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu. Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa. Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu. Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu. Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize.
Wolemekezeka Mulungu, amene sanandipatutsire ine pemphero langa, kapena chifundo chake.
Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga; pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.
Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.
Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu. Ndipo ndinati, Chindiwawa ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba. Ndidzakumbukira zimene adazichita Yehova; inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu. Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu; Mulungu wamkulu ndani monga Mulungu? Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu. Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe. Madziwo anakuonani Mulungu; anakuonani madziwo; anachita mantha, zozama zomwe zinanjenjemera. Makongwa anatsanula madzi; thambo lidamvetsa liu lake; mivi yanu yomwe inatulukira. Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka. Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nkumadzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike. Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.
Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo. Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye;
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.