Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 5:11 - Buku Lopatulika

11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 5:11
18 Mawu Ofanana  

muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.


Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova.


Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.


Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira.


Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.


Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa