Masalimo 5:10 - Buku Lopatulika10 Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu. Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe, muŵachotse pamaso panu chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri, chifukwa akuukirani Inu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu! Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo. Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri, pakuti awukira Inu. Onani mutuwo |
Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake.