Masalimo 5 - Buku LopatulikaMatsoka a oipa, madalitso a olungama Kwa Mkulu wa Nyimbo: aimbire zitoliro. Salimo la Davide. 1 Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga. 2 Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera. 3 M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira. 4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu. 5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu, mudana nao onse akuchita zopanda pake. 6 Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye. 7 Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu. 8 Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga. 9 Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo. 10 Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu. 11 Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu. 12 Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi