Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 5:3 - Buku Lopatulika

3 M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 5:3
15 Mawu Ofanana  

M'mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka; ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.


Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu.


Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.


Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.


Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.


Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.


Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga.


Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.


Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.


Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu; akulemekezani chilemekezere.


Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova, ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.


Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.


munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine.


Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa