Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:7 - Buku Lopatulika

7 Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:7
24 Mawu Ofanana  

Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mzinda wa Susa unadodoma.


Inde mungakhale munena, Sindimpenya, mlanduwo uli pamaso pake, ndipo mumlindira.


Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.


Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.


Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.


Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.


Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika.


Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja.


Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa