Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:8 - Buku Lopatulika

8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali, usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:8
18 Mawu Ofanana  

Tsono Farao anati kwa iye, Koma chikusowa iwe nchiyani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.


Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako, kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe? Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwake?


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza.


Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


ndikadati, Ndidzafotokozera chotere, taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.


Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Koma sikudakomere Yona konse, ndipo anapsa mtima.


Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.


Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,


Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.


Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa