Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha, chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:6
10 Mawu Ofanana  

Ndipo moyo wako udzayera koposa usana; kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa.


Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.


Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.


ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;


Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.


Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire mu Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa