Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 36:5 - Buku Lopatulika

5 Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 36:5
14 Mawu Ofanana  

ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi.


Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.


Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.


Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.


Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.


Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.


Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao;


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mzinda muno;


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa