Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 36:4 - Buku Lopatulika

4 Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Amaganiza zachiwembu akamagona usiku. Amayenda pa njira imene siili yabwino, sapewa zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa; iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo ndipo sakana cholakwa chilichonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 36:4
24 Mawu Ofanana  

Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.


Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupachika Mordekai pamtengo adaukonzeratu.


Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.


Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.


Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo,


Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.


pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu.


Izinso zili za anzeru, poweruza chetera silili labwino.


Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.


Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao;


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo.


Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;


amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.


Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.


Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;


Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa