Masalimo 36 - Buku LopatulikaKuipitsitsa kwa anthu, kukometsetsa kwa Mulungu Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. 1 Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake. 2 Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho. 3 Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino. 4 Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho. 5 Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo. 6 Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama. 7 Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu. 8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu. 9 Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika. 10 Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima. 11 Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse. 12 Pomwepo padagwera ochita zopanda pake. Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi