Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 36:1 - Buku Lopatulika

1 Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Uchimo umalankhula mu mtima wa munthu wosamvera Mulungu. Alibe mantha ndi Mulungu m'maganizo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Uthenga uli mu mtima mwanga wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa: Mu mtima mwake mulibe kuopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 36:1
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.


Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.


Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.


Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.


Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.


Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.


Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.


Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao.


Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova.


Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,


Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:


Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:


Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa