Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 36:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Amadzinyenga m'maganizo mwake, kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira ndi kudana nalo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri, sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 36:2
15 Mawu Ofanana  

Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo, ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani?


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;


Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.


Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa