Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 9:10 - Buku Lopatulika

10 ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 9:10
24 Mawu Ofanana  

Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.


Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.


Ine sindinanene m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.


Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.


Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.


Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa