Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 4:1 - Buku Lopatulika

1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga. Mudabwera kudzandithandiza pamene ndinali m'mavuto. Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 4:1
35 Mawu Ofanana  

Inde akadakukopani muchoke posaukira, mulowe kuchitando kopanda chopsinja; ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu.


Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.


Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga.


Yehova asunga opusa; ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.


Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu.


Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.


Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.


Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?


Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.


Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika.


Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.


Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.


Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.


Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.


Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange muukali wanu.


Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake;


Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;


Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa