Masalimo 4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa ChaleroSalimo 4 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. 1 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa. 2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela. 3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana. 4 Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela 5 Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova. 6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova. 7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano. 8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino. |
The Word of God in Contemporary Chichewa
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®
Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®
Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Biblica, Inc.