Masalimo 4 - Buku LopatulikaPemphero posautsidwa Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Salimo la Davide. 1 Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa. 2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti? 3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye. 4 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete. 5 Iphani nsembe za chilungamo, ndipo mumkhulupirire Yehova. 6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. 7 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao. 8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi