Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 4:8 - Buku Lopatulika

8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 4:8
16 Mawu Ofanana  

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.


Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa.


Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.


Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.


Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.


amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa