Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 4:2 - Buku Lopatulika

2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu inu, mudzaleka liti kunyoza ulemu wanga? Bwanji mukukondabe zinthu zachabechabe? Bwanji mukulakalakabe zinthu zonama?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 4:2
29 Mawu Ofanana  

M'mwemo anasintha ulemerero wao ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu.


Munyazitsa uphungu wa wozunzika, koma Yehova ndiye pothawira pake.


Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake?


Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.


Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama, koma ndikhulupirira Yehova.


Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?


Oipa achita chilendo chibadwire, asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.


Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.


Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo, ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.


Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.


Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.


kuti monga mwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.


Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.


musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa