Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 4:6 - Buku Lopatulika

6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Alipo ambiri amene amati, “Ndani angatiwonetse zabwino? Mutiyang'ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 4:6
20 Mawu Ofanana  

Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu.


Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse; mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake;


Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.


ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo.


Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.


Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.


Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;


Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri; apo adzaphera nsembe za chilungamo; popeza adzayamwa zochuluka za m'nyanja, ndi chuma chobisika mumchenga.


Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa