Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 42:8 - Buku Lopatulika

8 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake, nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane; pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 42:8
20 Mawu Ofanana  

Pakuti mafunde a imfa anandizinga, mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.


Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga, wakupatsa nyimbo usiku;


Akadatimiza madziwo, mtsinje ukadapita pa moyo wathu;


Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.


Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao.


Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.


Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu; lamulirani chipulumutso cha Yakobo.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.


Ndikumbukira nyimbo yanga usiku; ndilingalira mumtima mwanga; mzimu wanga unasanthula.


Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.


Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.


pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.


Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.


Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.


Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;


Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.


Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa