Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 42:9 - Buku Lopatulika

9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndimafunsa Mulungu, thanthwe langa, kuti, “Mwandiiŵaliranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 42:9
19 Mawu Ofanana  

Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.


Ndapindika, ndawerama kwakukulu; ndimayenda woliralira tsiku lonse.


Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?


chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.


Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.


Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?


Ndipo anakumbukira kuti Mulungu ndiye thanthwe lao, ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao.


Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.


Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.


Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.


Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israele, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira?


Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa