Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 42:10 - Buku Lopatulika

10 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo pamene adani anga akundinyoza, tsiku lonse akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 42:10
8 Mawu Ofanana  

Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?


Mtima wanga uwawa m'kati mwanga; ndipo zoopsa za imfa zandigwera.


Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.


Bwanji mutiiwala chiiwalire, ndi kutisiya masiku ambirimbiri.


Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa