Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 119:9 - Buku Lopatulika

9 Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:9
29 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.


Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


Pakuti mundilembera zinthu zowawa, ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga.


Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga.


Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.


Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.


Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.


kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;


kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza;


Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha;


ndinazindikira pakati pa aang'ono mnyamata wopanda nzeru,


Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.


Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu.


Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi;


Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.


Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa