Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 63:1 - Buku Lopatulika

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 63:1
37 Mawu Ofanana  

Ona ndidzaima pa madooko a m'chipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.


Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; maweruzo ake akhala padziko lonse lapansi.


koma ukafunitsitsa Mulungu, ndi kupembedza Wamphamvuyonse;


Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.


Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu: Ndinayembekezera mau anu.


Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.


Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.


Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.


Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.


Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


Akundikonda ndiwakonda; akundifunafuna adzandipeza.


Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.


Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.


Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.


Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.


Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.


Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.


Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.


Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; chokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa