Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI A ANYAMATA NDI ATSIKANA

MAVESI A ANYAMATA NDI ATSIKANA

Ana inu, ana ndi dalitso lochokera kwa Mulungu. Tiyenera kuwaphunzitsa mawu a Mulungu kuyambira ali aang'ono, kuwaphunzitsa kumuopa Iye. Akakumana ndi mavuto m'moyo wawo, adzakumbukira zimene anaphunzira ndipo adzafuna Mulungu.

Ambuye Yesu amakonda ana, ndipo amatiuza ife akuluakulu kuti tikhale ngati iwo kuti tilowe mu ufumu wakumwamba. Monga mmene Baibulo limatiuza, “Yesu anati: Lolani ana aang’ono abwere kwa Ine, musawaletse; pakuti ufumu wakumwamba uli wa otere.” (Mateyu 19:14)

Mtima woyera wa mwana, kudzichepetsa kwawo, ndi mmene amamvekelera msanga kukhululukira ena, ndi makhalidwe abwino amene ana ali nawo, ndipo Mulungu amawakonda chifukwa cha zimenezi. Tiyenera kusamalira makhalidwe amenewa mwa kuwaphunzitsa mawu a Mulungu usana ndi usiku. “Unikire mwana njira yoyenera iye; angakhale wokalamba sadzachoka m’menemo.” (Miyambo 22:6)




Luka 18:16

Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:3

nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:16

nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:2

M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38-39

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:4

Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:15

Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:33

Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 18:8

Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:4

Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:27

Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:12

popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:15-17

Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:14

Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41

Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47-48

Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:14

amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:13

Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:5

Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26-27

Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:9

kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1-3

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai. Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho. Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima. Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye; chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo. Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:21

chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:16

Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:21

Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:12

Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:18

Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 22:16

Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5

Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:6

Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:33

Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:6

nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:30

Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:3

Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:10

ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:10

Chibadwire ine anandisiyira Inu, kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:3

Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:25

Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:25

Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18

Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:17

Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:15

Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:2

nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:19

Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 148:12-13

Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:17

ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5

Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera ulemerero ndi kulambiridwa konse. Ndimadzera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndikulengeza kuti mudzakwaniritsa chifuniro chanu mwa iwo ndipo adzakhala amuna ndi akazi ogwirizana ndi mtima wanu, omvera Inu ndi olemekeza makolo awo. Ambuye, ikani m'badwo wa makolo odzipereka kwa Inu kuti aphunzitse ana awo m'njira zanu. Ndikukupemphani kuti muwasunge polowa ndi potuluka ndipo atetezedwe ku ziwembu zonse ndi misampha ya mdani. Pangani mitima yawo Ambuye, awathandizeni kukula tsiku ndi tsiku msinkhu, chisomo ndi nzeru, kuti akhale ndi unyamata wodzipereka kwa Inu. M'mawu anu mukuti: Yesu anati: “Lolani ana aang’ono abwere kwa Ine, musawaletse, pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wa anthu onga iwowa.” Mzimu Woyera, awathandizeni kukhala olimba mtima kuti agonjetse mantha, apambane mayesero ndi kupita patsogolo tsiku ndi tsiku m’zimene mwandikonzera Ine, awathandizeni kuti asadetsedwe ndi dziko lino, koma akhazikitse mitima yawo kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Inu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa