Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 5:6 - Buku Lopatulika

6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Uyu ndiye anabwera mwa madzi ndi magazi, ndiye Yesu Khristu. Sanabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi magazi. Ndipo ndi Mzimu Woyera amene akuchitira umboni, chifukwa Mzimu Woyera ndi choonadi.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 5:6
39 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.


Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.


pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.


Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.


ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.


Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.


Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?


amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;


Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,


popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse;


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu,


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa