Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:12 - Buku Lopatulika

12 Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:12
22 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.


Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.


kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;


Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.


Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.


Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.


ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.


ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;


Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.


pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.


Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa