Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Simoni uja nayenso adakhulupirira, ndipo atabatizidwa, ankakhalira limodzi ndi Filipo. Adazizwa pakuwona zizindikiro ndi zozizwitsa zimene zinkachitika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:13
16 Mawu Ofanana  

Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.


nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.


Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse.


Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kumva mau a Mulungu.


Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pazokha ndi manja a Paulo;


namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Chipata Chokongola cha Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.


Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa