Yohane 1:33 - Buku Lopatulika33 Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ndipo sindinamdziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’ Onani mutuwo |