Nehemiya 9:25 - Buku Lopatulika25 Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Iwo analanda mizinda yotetezedwa ndi dziko lachonde. Anatenganso nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime zokumbidwa kale, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndi mitengo yambiri ya zipatso. Ndipo anadya nakhuta ndipo anali athanzi. Choncho ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu wopambana. Onani mutuwo |