Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:24 - Buku Lopatulika

24 Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Choncho zidzukulu zaozo zidaloŵamo ndi kukhazikika m'menemo, ndipo Inu mukuŵatsogolera, mudagonjetsa Akanani, nzika za m'dzikomo. Akananiwo, ndiye kuti mafumu ao ndi anthu onse am'dzikomo, mudaŵapereka kwa anthu anu, kuti achite nawo monga angafunire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Choncho zidzukulu zawo zinapita ndi kukalandira dzikolo. Inu munagonjetsa pamaso pawo, Akanaani amene amakhala mʼdzikolo. Inde munapereka mʼmanja mwawo mafumu awo pamodzi ndi anthu a mʼdzikomo kuti achite nawo monga angafunire.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:24
13 Mawu Ofanana  

Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake.


Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.


Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana.


ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.


Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.


Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.


mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;


mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m'mwemo.


Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.


Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa