Masalimo 138 - Buku LopatulikaDavide ayamika Mulungu pa kukhulupirika kwake, naneneratu kuti mafumu onse adzatero Salimo la Davide. 1 Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu. 2 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse. 3 Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga. 4 Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu. 5 Ndipo adzaimbira njira za Yehova; pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu. 6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali. 7 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa. 8 Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi