Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 138:2 - Buku Lopatulika

2 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 138:2
27 Mawu Ofanana  

Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,


Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.


wakusungira mtumiki wanu Davide atate wanga chimene mudamlonjezacho; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.


Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.


Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.


Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?


Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake: Iye ndiye Woyera.


Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.


Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa