Masalimo 28 - Buku LopatulikaApempha chipulumutso, ayamika populumutsidwa Salimo la Davide. 1 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda. 2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera. 3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa. 4 Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo. 5 Pakuti sasamala ntchito za Yehova, kapena machitidwe a manja ake, adzawapasula, osawamanganso. 6 Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga. 7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga. 8 Yehova ndiye mphamvu yao, inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake. 9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi