Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 28:4 - Buku Lopatulika

4 Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao, muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita. Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao, Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo ndi ntchito zawo zoyipa; abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 28:4
19 Mawu Ofanana  

Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;


Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.


Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa padziko lapansi, ndi mbeu zao mwa ana a anthu.


Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu.


Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.


Mudzawabwezera chilango, Yehova, monga mwa machitidwe a manja ao.


Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,


Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.


Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;


Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m'chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza.


Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa