Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 28:3 - Buku Lopatulika

3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 28:3
17 Mawu Ofanana  

Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.


Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;


Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza.


Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;


Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa