Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 28:2 - Buku Lopatulika

2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Imvani kupempha kwanga, pamene ndikulirira Inu kuti mundithandize, pamene ndikukupembedzani pokweza manja anga ku malo anu opatulika kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 28:2
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anakonza m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuikamo likasa la chipangano la Yehova.


Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kachisi, ndi chipinda chamkati; namanga zipinda zozinga.


tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;


Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m'litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;


Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.


Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.


Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova.


Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.


Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.


Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.


Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.


Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Daniele alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake.


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa