Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 28:7 - Buku Lopatulika

7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 28:7
36 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Ndidzaimbira Yehova, pakuti anandichitira zokoma.


Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.


Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!


Makolo athu anakhulupirira Inu; anakhulupirira, ndipo munawalanditsa.


Yehova ndiye mphamvu yao, inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.


Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.


Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera.


Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.


Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.


Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira, ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa