Masalimo 92 - Buku LopatulikaAnthu onse ayamike Mulungu chifukwa cha ntchito zake, chilungamo chake, ndi chifundo chake Salimo, Nyimbo ya pa Sabata. 1 Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. 2 Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse. 3 Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake. 4 Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu. 5 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu. 6 Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi; 7 chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha. 8 Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse. 9 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika. 10 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. 11 Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. 12 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. 13 Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. 14 Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, 15 kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi